MUTU 10
Yesetsani Kuti Banja Lanu Lizikondweretsa Mulungu
1. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova kawirikawiri amakhala ndi mabanja osangalala?
ANTHU a Mboni za Yehova amadziwika kuti amakhala ndi mabanja osangalala. Mwachitsanzo, mphunzitsi wina wa pa yunivesite ya Oxford, dzina lake Bryan Wilson, analemba kuti: “A Mboni amapereka malangizo osiyanasiyana othandiza kwambiri . . . monga okhudza moyo wa banja, makhalidwe abwino, kulera ana ndi nkhani zina. Iwo amapereka malangizo ambiri othandiza, omwe ndi ochokera m’Malemba Opatulika. Malangizowa ndi ogwirizana ndi mfundo zimene anthu amaona kuti n’zothandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku.” Mosakayikira, inuyo mwaphunzira zambiri m’Mawu a Mulungu zokhudza mmene anthu angakhalire ndi banja losangalala.
2. (a) Kodi mwaona kuti chikuchitika n’chiyani m’mabanja ambiri masiku ano? (b) Kodi tikambirana mabuku a m’Baibulo ati kuti tipeze malangizo othandiza m’banja?
2 Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, Satana akuchititsa kuti mabanja azikumana ndi mavuto osiyanasiyana. Izi zachititsa kuti anthu a m’banja limodzi asamakhulupirirane, ndipo zimenezi zinkachitikanso m’nthawi ya Mika. Iye analemba kuti: “Musamakhulupirire anzanu.” Ndipo anapitiriza kuti: “Samala zonena zako polankhula ndi amene umagona naye pafupi. Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi. Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.” (Mika 7:5, 6) Mukukhala m’dziko limene mabanja ambiri sakuyenda bwino, koma inuyo mukuyesetsa mwakhama kuti zoterezi zisachitike m’banja lanu. Zimenezi zachititsa kuti banja lanu liziyenda bwino komanso lizikondweretsa kwambiri Mulungu. N’kutheka kuti izi zatheka chifukwa choti mumagwiritsa ntchito mfundo za m’malemba, monga zopezeka pa Deuteronomo 6:5-9, Aefeso 5:22-33, 6:1-4 ndiponso Akolose 3:18-21. Koma kodi munayamba mwaganizirapo kuti m’mabuku 12 a aneneri mungapezemo malangizo okuthandizani kukhala ndi banja losangalala? M’mutu uno, tikambirana zitsanzo zingapo za malangizo amenewa. Koma pali zinanso zoti muchite kuwonjezera pa kuphunzira malangizo amenewa. Yesani kuona mmene zitsanzo zimenezi zingakuthandizireni kuti mupeze mfundo zina zothandiza. Kumapeto kwa mutu uno kuli malemba amene angakuthandizeni kuona zimene mungaphunzire m’mabuku 12 amenewa.
“INE NDIMADANA NDI ZAKUTI ANTHU AZITHETSA MABANJA”
3, 4. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano amachita chiyani pofuna kupewa mavuto a m’banja? (b) Kodi anthu ankakonda kuchita chiyani pa nkhani ya ukwati m’nthawi ya Malaki?
3 Choyamba, tiyeni tikambirane za mgwirizano wa mwamuna ndi mkazi wake. Kale, anthu ambiri ankaona kuti kuthetsa ukwati si njira yabwino yopewera mavuto a m’banja. Ndipotu kuthetsa ukwati sinali nkhani ya masewera. Mwachitsanzo, ku England m’zaka za m’ma 1800, nyumba ya malamulo inkafunika kuti ivomereze kaye munthu asanathetse ukwati wake. Zimenezi zinkathandiza kuti mabanja asamathe mwachisawawa. Koma masiku ano zinthu zasintha. Buku lina linanena kuti: “Chiwerengero cha mabanja amene akhala akutha kuyambira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, chakhala chikukwera modetsa nkhawa m’mayiko ambiri. . . . Anthu asintha kwambiri mmene amaonera nkhani yothetsa ukwati . . . moti akuona kuti palibe vuto lililonse ndi kuthetsa ukwati.” (Encyclopædia Britannica) Maukwati ambiri akutha ngakhale m’mayiko ngati Korea, kumene zaka zoposa 10 zapitazo, anthu ankadana ndi munthu aliyense wothetsa ukwati. Masiku ano, anthu m’mayiko ambiri akuona kuti kuthetsa ukwati ndi njira yabwino yopewera mavuto ngati banja silikuyenda bwino.
4 M’nthawi ya Malaki, cha m’ma 400 B.C.E., Ayuda ambiri ankathetsa mabanja awo. Malaki anawauza kuti: “Yehova wakudzudzulani popeza kuti aliyense wa inu wachitira zachinyengo mkazi amene anamukwatira ali mnyamata.” Popeza kuti amuna ambiri ankachita zachinyengo, paguwa la Yehova panadzaza misozi ya akazi amene anali “kulira ndi kubuula” chifukwa chochitiridwa zachinyengozo. Ndipo ansembe, omwe anali okonda ziphuphu, ankalekerera nkhanza zimenezi.—Malaki 2:13, 14.
5. (a) Kodi Yehova amaona bwanji nkhani yothetsa ukwati? (b) N’chifukwa chiyani kuchitira mwamuna kapena mkazi wanu zachinyengo ili nkhani yaikulu?
5 Kodi Yehova ankaona bwanji nkhani yothetsa banja m’nthawi ya Malaki? Mneneri Malaki analemba kuti: “‘Ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja,’ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli.” Mneneriyu ananenanso kuti Yehova ‘sanasinthe.’ (Malaki 2:16; 3:6) Kodi mfundoyi ikutanthauza chiyani? Kale kwambiri, Mulungu anali atasonyeza kuti amadana ndi kuthetsa ukwati. (Genesis 2:18) Ankadananso ndi zimenezi m’nthawi ya Malaki ndipo amadana nazonso masiku ano. Anthu ena amaganiza zothetsa ukwati chifukwa choti sakusangalala ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Komabe ngakhale kuti iwo angapezere mnzawoyo zifukwa zina mwachinyengo, Yehova amafufuza mitima yawo. (Yeremiya 17:9, 10) Iye amadziwa chinyengo chilichonse chimene munthu angachite kuti athetse banja lake, ngakhale atayesa kupereka zifukwa zina. Izi zili choncho “chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.”—Aheberi 4:13.
6. (a) Kodi kuona nkhani yokhudza kuthetsa ukwati ngati mmene Yehova amaionera kungakuthandizeni bwanji? (b) Kodi mfundo yaikulu inali iti pamene Yesu ankapereka malangizo pa nkhani yothetsa ukwati?
6 Mwina inuyo simukukumana ndi mavuto amene angachititse kuti banja lanu lithe, komabe muyenera kukumbukira mmene Yehova amaonera nkhani yothetsa ukwati. Palibe munthu wangwiro, choncho tingayembekezere kuti m’banja mungakhale mavuto kapena kusemphana maganizo. Koma kodi mungaganize zoti njira yabwino yothetsera mavutowo n’kuthetsa ukwati? Kodi pamene mukukangana ndi mwamuna kapena mkazi wanu, ndi bwino kunena zoti banja lingotha? Ambiri amachita zimenezi, koma Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana aziyesetsa kupeza njira zabwino zothetsera mavuto a m’banja lawo. Ndipotu Yesu Khristu ananena kuti pali chifukwa chimodzi chokha chovomerezeka chimene chingachititse kuti banja lithe. Chifukwacho ndi dama, kapena kuti kugonana ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu. Komabe, kodi mfundo yaikulu m’malangizo a Yesu inali yotani? Iye anauza anthu amene ankamumvetsera kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” Apa Yesu anabwereza mfundo yosasintha yochokera kwa Yehova, imene Malaki anali atanena zaka pafupifupi 450 m’mbuyomo.—Mateyu 19:3-9.
7. Mogwirizana ndi malangizo amene ali m’buku la Malaki, kodi mungatani kuti banja lanu likhale lolimba?
7 Ndiyeno kodi Akhristu okwatirana angatani kuti azikondana kwambiri? Malaki anatchula njira imodzi yothandiza kwambiri. Iye anati: “Musamale ndi maganizo a mumtima mwanu ndipo musamachite zachinyengo.” (Malaki 2:16) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kutetezera mtima wathu, womwe ungatichititse zinthu zoipa. Ngati tikuteteza ‘maganizo a mumtima mwathu,’ tidzapewa kuyang’anitsitsa mwamuna kapena mkazi amene sitinakwatirane naye. (Mateyu 5:28) Mwachitsanzo, mwina tingamasangalale mumtima mwathu ngati munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wathu akutisonyeza chidwi. Zimenezi zingasonyeze kuti sitikuteteza maganizo a mumtima mwathu. Choncho, mfundo yofunika kwambiri imene tikuphunzira m’mabuku 12 a aneneri, ndi yakuti tiyenera kuteteza ‘maganizo a mumtima mwathu.’ Mfundo imeneyi ingathandize kuti banja lathu likhale lolimba.
8, 9.N’chifukwa chiyani nkhani ya Hoseya ndi Gomeri inalembedwa m’Baibulo?
8 Mosakayikira, inuyo mukufunitsitsa kuti banja lanu liziyenda bwino. Komabe, simungapeweretu mavuto onse a m’banja. Ndiyeno kodi mungatani kuti muzithana ndi mavutowo m’njira yabwino, makamaka ngati mukuona kuti mnzanuyo ndi amene amayambitsa mavuto ambiri? Kumbukirani nkhani ya Hoseya, imene yatchulidwa m’buku lino, m’Mutu 2 ndi 4. Mkazi wake Gomeri anayamba kuchita “dama” ndipo ‘ankathamangira amuna’ amene ankachita nawo damawo. Kenako Hoseya anamusiya ndipo mkaziyu anayamba kuvutika ngati kapolo. Koma Hoseya anatenganso Gomeri n’kukhala mkazi wake, ndipo Yehova anamuuza kuti azikonda mkazi wakeyo. Hoseya anachita zimenezi atapereka ndalama kwa mwamuna wina amene ankakhala ndi Gomeri ngati mkazi wake. N’chifukwa chiyani Hoseya anauzidwa kuti achite zimenezi? Yehova ankafuna kusonyeza bwino zimene zinkachitika pakati pa iyeyo ndi Aisiraeli. Yehova anali “mwamuna” wa Aisiraeliwo, ndipo iwo anali ngati mkazi wake.—Hoseya 1:2-9; 2:5-7; 3:1-5; Yeremiya 3:14; Yesaya 62:4, 5.
9 Kuyambira kale, Aisiraeli ankakhumudwitsa Yehova chifukwa cholambira milungu ina. (Ekisodo 32:7-10; Oweruza 8:33; 10:6; Salimo 78:40, 41; Yesaya 63:10) Ufumu wa kumpoto wa mafuko 10 unali ndi mlandu chifukwa cholambira mafano a mwana wa ng’ombe. (1 Mafumu 12:28-30) Kuwonjezera pamenepa, Aisiraeli sankadalira Yehova amene anali ngati mwamuna wawo, koma ankadalira maufumu ena omwe ankachita nawo dama. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iwo anayamba kupita kukachita dama ndi Asuri ndipo anali ngati mbidzi yosamva. (Hoseya 8:9) Ndiyeno kodi inuyo mungamve bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu atachita zimenezi?
10, 11. Kodi mungatsanzire bwanji Yehova ngati m’banja mwanu muli mavuto ndipo zikuoneka kuti mnzanuyo ndiye wolakwa?
10 Pofika m’nthawi ya Hoseya, panali patadutsa zaka zoposa 700 kuchokera pamene Aisiraeli anachita pangano ndi Yehova. Komabe, Mulungu anali wokonzeka kuwakhululukira ngati anthuwo akanabwerera kwa iye. Zikuoneka kuti Hoseya anayamba utumiki wake monga mneneri chisanafike chaka cha 803 B.C.E. Izi zikusonyeza kuti Yehova anapitiriza kulezera mtima Aisiraeli kwa zaka zina pafupifupi 60, ndipo Ayuda, kwa zaka zina pafupifupi 200. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mmene zinthu zinalili m’banja la Hoseya, Yehova anapitiriza kupempha anthu ake amene anachita nawo panganowo kuti alape. Yehova anali ndi zifukwa zomveka zothetsera ukwati wake ndi Isiraeli. Komabe, iye anapitiriza kutumiza aneneri kuti akathandize mkazi wake wophiphiritsayo kuti abwerere kwa iye, ngakhale kuti zimenezi zinali zopweteka kwambiri.—Hoseya 14:1, 2; Amosi 2:11.
11 Tiyerekezere kuti m’banja mwanu muli mavuto ndipo zikuoneka kuti mnzanuyo ndi amene walakwa, kodi mungachite zinthu ngati mmene Yehova anachitira? Kodi mungayesetse kuchita zinthu zothandiza kuti banja lanu liziyenda bwino ngati kale? (Akolose 3:12, 13) Pangafunike kudzichepetsa kuti muchite zimenezi. Ndipotu Yehova anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa zimene anachitira Aisiraeli. (Salimo 18:35; 113:5-8) Mulungu ‘analankhula’ ndi Aisiraeli ‘mowafika pamtima’ powachonderera kuti abwerere kwa iye. Popeza kuti ndife anthu opanda ungwiro, tili ndi chifukwa chomveka cholankhulira ndi mwamuna kapena mkazi wathu momufika pamtima poyesetsa kuthetsa mavuto kapena zolakwika zina m’banja. N’zolimbikitsa kuona kuti Aisiraeli anasintha Yehova atayesetsa kuwathandiza. Nawonso Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo analapa, kenako anabwerera kwawo ndipo ankatcha Yehova kuti “Mwamuna wanga.”—Hoseya 2:14-16.a
12. Kodi kuganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi mkazi wake wophiphiritsa kungathandize bwanji kuti banja lanu liziyenda bwino?
12 M’banja mwanu mukabuka vuto lalikulu, muziyesetsa mwakhama kulithetsa kuti banja lanu lipitirize kuyenda bwino. Mulungu anali wokonzeka kukhululuka tchimo la dama limene mkazi wake wophiphiritsa ankachita. Mavuto ambiri amene Akhristu oona amakumana nawo m’banja si aakulu kwambiri ngati mmene tchimo la Aisiraeliwo linalili. Mavuto ambiri amayamba ngati wina walankhula mawu okhadzula. Choncho ngati mwakhumudwa ndi mawu amene mkazi kapena mwamuna wanu walankhula, muziganizira zimene zinachitikira Hoseya komanso Yehova. (Miyambo 12:18) Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhululukire mnzanuyo.
13. Kodi tikuphunzirapo chiyani tikaganizira zoti Yehova ankafuna kuti anthu ake omwe ankachita zoipa alape?
13 Pali mfundo inanso imene tingaphunzire pa nkhaniyi. Mulungu ankafunitsitsa kuti anthu ake akhale nayenso pa ubwenzi. Koma kuti zimenezi zitheke, anthuwo anafunika kusiya dama. Ponena za Aisiraeli omwe ankachita damawo, Mulungu anauza Hoseya kuti: ‘Asiye dama lawo ndi chigololo chawo.’ (Hoseya 2:2) Anthuwo anafunika kulapa ndiponso ‘kubala zipatso zosonyeza kulapa.’ (Mateyu 3:8) Mfundo imeneyi ingakuthandizeni kuti muziganizira kwambiri za zolakwa zanu osati za mwamuna kapena mkazi wanu. Ndiye ngati mwalakwira mnzanuyo, bwanji osayesetsa kupepesa moona mtima komanso kusintha zimene mwalakwitsazo n’cholinga choti banja lanu liziyenda bwino? Kuchita zimenezi kungathandize kuti mnzanuyo akukhululukireni.
PEREKANI MALANGIZO “MWACHIKONDI”
14, 15. (a) Malinga ndi lemba la Malaki 4:1, n’chifukwa chiyani simuyenera kuona mopepuka udindo wanu wophunzitsa ana anu? (b) Kodi mungatani kuti muthandize ana anu kudziwa Yehova?
14 Tingaphunzire mfundo zambiri zokhudza moyo wa banja tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli, zomwe zafotokozedwa m’mabuku 12 a aneneri. M’mabukuwa muli mfundo zimene zingakuthandizeni kulera bwino ana anu. Koma kunena zoona, kulera ana masiku ano si ntchito yamasewera. Ndipotu makolo ayenera kuona udindo wawo kuti ndiwofunika kwambiri. Baibulo limati: “‘Tsiku limene likubweralo lidzawanyeketsa moti pa iwo sipadzatsala mizu kapena nthambi,’ watero Yehova wa makamu.” (Malaki 4:1) Pa tsiku lalikulu limenelo, Yehova adzaweruza mwachilungamo ana aang’ono (kapena kuti nthambi) potengera zochita za makolo awo (kapena kuti mizu), omwe ali ndi udindo wowasamalira. (Yesaya 37:31) Zimene makolo akuchita pa moyo wawo zingachititse kuti ana awo aang’ono adzapeze madalitso m’tsogolo muno kapena ayi. (Hoseya 13:16) Ngati inuyo makolo (mizu) simuli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kodi mukuganiza kuti n’chiyani chidzachitikire ana anu aang’ono (nthambi) pa tsiku la mkwiyo wa Yehova? (Zefaniya 1:14-18; Aefeso 6:4; Afilipi 2:12) Koma ngati mukuyesetsa mwakhama kuchita zinthu zimene Mulungu amafuna, zingachititse kuti ana anu aang’ono adzapeze madalitso.—1 Akorinto 7:14.
15 Mtumwi Paulo atagwira mawu ulosi wa Yoweli wonena za kuitana pa dzina la Yehova, analemba kuti: “Kodi angaitane bwanji munthu amene samukhulupirira? Angakhulupirire bwanji munthu amene sanamvepo za iye?” (Aroma 10:14-17; Yoweli 2:32) Ngakhale kuti Paulo ankanena za ntchito yathu yolalikira, mfundoyi ingagwirenso ntchito pa nkhani yophunzitsa ana anu. Kodi ana anu angakhulupirire bwanji Yehova asanamve za iye? Kodi tsiku ndi tsiku mumapatula nthawi kuti muphunzitse ana anu kuti adziwe zoti Yehova ndi wabwino? Kodi mumawathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova komanso malamulo ake? Nthawi zambiri ana amakula bwino ngati nthawi zonse makolo amawaphunzitsa za Yehova.—Deuteronomo 6:7-9.
16. Mogwirizana ndi lemba la Mika 6:3-5, kodi mungatsanzire bwanji Yehova mukamalangiza ana anu?
16 Nthawi zambiri ana akakhala aang’ono, zimakhala zosavuta kupita nawo kumisonkhano yachikhristu. Koma akamakula, amayamba kuchita zinthu pawokha. Kodi mungatani kuti muthandize mwana wanu ngati nthawi zina amachita zinthu zosonyeza kusamvera? Mabuku 12 a aneneri angakuthandizeni, makamaka mukaona mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli komanso Ayuda. (Zekariya 7:11, 12) Mwachitsanzo, taonani mawu amene Yehova anagwiritsa ntchito polankhula ndi Aisiraeli, palemba la Mika 6:3-5. Mulungu anawatchula kuti “anthu anga,” ngakhale kuti iwo anali ochimwa. Iye anawachonderera kuti: “Inu anthu anga, chonde kumbukirani.” M’malo mowadzudzula mwaukali, Yehova anayesetsa kulankhula nawo mowafika pamtima. Kodi nanunso simungayesetse kutsanzira Yehova, ngakhale pamene mwanayo walakwa? Ngakhale mwanayo atalakwa kwambiri, mulangizeni kapena m’patseni chilango mwachikondi monga munthu wofunika m’banja lanu, ndipo pewani kumunyoza. Yesetsani kumuchonderera mwachikondi m’malo momukalipira. Mufunseni mafunso amene angathandize kuti anene maganizo ake. Komanso yesetsani kulankhula momufika pamtima kuti nayenso alankhule momasuka.—Miyambo 20:5.
17, 18. (a) N’chiyani chomwe chingakuchititseni kupereka chilango kwa ana anu? (b) Kodi mungatani kuti mupitirize kuchita zinthu “mwachikondi” ndi ana anu?
17 N’chifukwa chiyani mumapereka chilango kwa ana anu? Makolo ena amachita zimenezi potetezera mbiri ya banja lawo. Kudzera mwa Hoseya, Yehova ananena cholinga chimene ankaperekera chilango kwa anthu ake. Iye anati: ‘Ndinaphunzitsa Efuraimu kuyenda, amenenso ndinamunyamula m’manja mwanga. Ndinali kumukoka mokoma mtima ndi mwachikondi.’ (Hoseya 11:3, 4) Apa Hoseya anayerekezera ubale umene unalipo pakati pa Yehova ndi Aisiraeli, ndi umene umakhala pakati pa bambo ndi mwana wake. Yerekezerani kuti mukuona bambo wachikondi amene wagwira dzanja la mwana wake pomuthandiza kuyenda. Bamboyo akuteteza mwanayo kuti asagwe komanso kuti asapite kutali n’kusochera.—Yeremiya 31:1-3.
18 Mungachite bwino kutsanzira Yehova pokonda ana anu ngati mmene iye ankakondera Aisiraeli. Mobwerezabwereza, Aisiraeli ankamusiya Yehova, koma iye sanasiye kuwatsogolera mwachikondi. Nthawi zina ana angakhumudwe ndi zinthu zing’onozing’ono komanso angayambe kusamvera, komabe pitirizani kuwakonda. Kumbukirani kuti Yehova sankakondera anthu ake akalakwa. Iye sankawalekerera koma ankawapatsa chilango mwachikondi ndipo ankawathandiza moleza mtima. Choncho mukaona kuti mwana wanu akusiya choonadi pang’onopang’ono, musanyalanyaze vutolo. Yesetsani kumubweza, ngati kuti mwamugwira dzanja, ndipo muzimuthandiza mwachikondi pa nthawi yovutayi. Muzipeza nthawi yocheza ndi mwana wanuyo komanso muzichita naye zinthu moleza mtima. Ndipotu simuyenera kunyalanyaza kuchita zimenezi chifukwa n’zofunika kwambiri.
19. N’chifukwa chiyani simuyenera kusiya kulangiza ana anu?
19 Hoseya ananeneratu kuti Aisiraeli amene anatengedwa kupita ku ukapolo, adzasintha pambuyo popatsidwa chilango. Iye anati: “Ana a Isiraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndiponso Davide mfumu yawo. Iwo adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzafunafuna ubwino wake m’masiku otsiriza.” (Hoseya 3:5) Zoonadi, chilango chimene Mulungu anapereka kwa anthu akewo chinathandiza kwambiri. Choncho musakayikire kuti chilango chimene inunso mungapereke kwa ana anu chidzawathandiza kwambiri. Yesani kuona makhalidwe abwino amene ana anu ali nawo. Muzilankhula nawo mokoma mtima, koma musalole kuti muphwanye mfundo za m’Baibulo pofuna kusangalatsa anawo. Ngakhale mwana wina atakana kutsatira malangizo anu ndipo akuoneka kuti ndi wosamvera, musataye mtima chifukwa nthawi ina akhoza kusintha.
PEWANI KUGWIRIZANA NDI ANTHU OIPA
20. Kodi ana angapeze yankho la funso liti m’mabuku 12 a aneneri, lokhudza anthu ocheza nawo?
20 Kodi ananu mungaphunzire chiyani m’mabuku 12 a aneneri? Mwina lemba limene makolo anu amagwiritsa ntchito kawirikawiri pokuthandizani kuti muzipewa kugwirizana ndi anthu oipa, ndi la 1 Akorinto 15:33. Koma n’kutheka kuti ena a inu mungafunse kuti: ‘Kodi kucheza ndi anthu amene salambira Yehova kuli ndi vuto lililonse?’ Mungapeze yankho la funso limeneli m’mabuku 12 a aneneriwa.
21-23. (a) Kodi achinyamata angaphunzire chiyani pa zimene Aedomu anachita? (b) Kodi ndani amene ali anzanu enieni?
21 Ngakhale kuti uthenga wa m’mabuku 12 a aneneri kwenikweni unkapita kwa anthu a Mulungu, uthenga wa m’buku la Obadiya unkapita kwa Aedomu, omwe ankadziwika kuti ndi abale enieni a Aisiraeli.b (Deuteronomo 2:4) Mosiyana ndi aneneri onse omwe analemba mabuku amenewa, Obadiya anagwiritsa ntchito mawu akuti “iwe” komanso “inu” polankhula ndi Aedomu. Ndiyeno ganizirani zimene Aedomuwo anachita cha m’ma 607 B.C.E., mzinda wa Yerusalemu utazunguliridwa ndi adani. Ngakhale kuti Aedomu anali abale enieni a Yakobo, iwo anagwirizana ndi Ababulo ndipo ankafuula kuti: “Fafanizani mzindawo! Ufafanizeni!” (Salimo 137:7; Obadiya 10, 12) Iwo ankasangalala chifukwa ankafuna kutenga dziko la Ayuda. Aedomu anafika podya chakudya ndi Ababulo, ndipo kuchita zimenezi kalelo nthawi zina kunkasonyeza kuti magulu awiriwo anachita pangano ndipo ali pa ubwenzi wabwino.
22 Taonani zimene Obadiya analosera zokhudza Aedomu. Iye anati: “Anthu onse [Ababulo] amene unachita nawo pangano akupusitsa . . . Anthu amene unali kukhala nawo mwamtendere akugonjetsa. Anthu amene ukudya nawo limodzi adzakutchera ukonde, ndipo udzakhala ngati munthu wosazindikira.” (Obadiya 7) Kodi n’chiyani chinachitikira Aedomu, amene anasiya m’bale wawo Yakobo, n’kugwirizana ndi Ababulo? Patapita nthawi, Ababulowo atayamba kulamuliridwa ndi Nabonidasi, anawononga Aedomu. Pofika m’nthawi ya Malaki, Mulungu anali atachititsa mapiri a Edomu kukhala bwinja, ndipo malo awo okhala anawasandutsa malo okhala mimbulu.—Malaki 1:3.
23 Tsopano ganizirani za anthu amene mumati ndi anzanu koma salambira Yehova. Mwina mwaonapo kuti ‘anyamata kapena atsikana omwe anachita pangano,’ kapena kuti amene amachezera limodzi, kawirikawiri ‘amatcherana ukonde’ ndipo amapusitsana. Nthawi zambiri zachinyengo zawozo zikadziwika, iwo anganene kuti mnzawo amene amuchitira zachinyengoyo ndi wosachangamuka, moti sankazindikira kuti akumuchitira zachinyengo. Zimenezi n’zofanana kwambiri ndi zimene Ababulo anachitira Aedomu. Kodi mukanakhalapo pa nthawiyo mukanasankha munthu wa ku Edomu kuti akhale mnzanu? Nanga bwanji masiku ano? Kodi mukuganiza kuti anthu omwe mumati ndi anzanuwo angakuthandizeni mutakumana ndi mavuto? (Obadiya 13-16) Ndiyeno ganizirani za Yehova Mulungu ndi anthu ake masiku ano. Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani nthawi iliyonse. Iye adzakuthandizani pa nthawi ya mavuto. Anthu akenso ndi ‘mabwenzi enieni amene amakukondani nthawi zonse,’ ndipo ndi okhulupirika moti “anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
UBWENZI WANU NDI YEHOVA NDI WAMTENGO WAPATALI
24, 25. Kodi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu chiyenera kukhala chiyani?
24 Zoonadi, ubwenzi wa anthu a m’banja limodzi ndi wofunika kwambiri ndipo ndi woyenera kuulimbitsa. Tingaphunzire zambiri pa ubwenzi woterewu kuchokera m’mabuku a aneneri 12. Mungachite bwino kuphunzira mabuku amenewa pogwiritsa ntchito buku lino. Mukachita zimenezi mupeza mfundo zambiri zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino. Koma kodi atumiki a Mulungu masiku ano amaona kuti nkhani yofunika kwambiri n’kukhala ndi banja losangalala basi?
25 Taonani mfundo ina yosangalatsa imene Yoweli ananena pamene ankalosera za tsiku la Yehova limene likubweralo. Iye anati: “Sonkhanitsani anthu onse pamodzi ndipo muyeretse mpingo. . . . Mkwati atuluke m’chipinda chake ndipo mkwatibwi atuluke kumalo ake ogona.” (Yoweli 2:15, 16) Anthu onse m’banja ankafunikira kusonkhanitsidwa pamodzi kuti alambire Yehova. Ngakhale anthu ongokwatirana kumene, omwe kawirikawiri amakhala otanganidwa, ankafunikiranso kusonkhanitsidwa. Choncho ifenso palibe chimene chiyenera kutilepheretsa kusonkhana pamodzi kuti tilambire Mulungu. Popeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi, tiyenera kuona ubwenzi wathu ndi Yehova kuti ndi wofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. M’gawo lomaliza la buku lino, tikambirana mfundo yakuti tiziyembekezera tsiku la Yehova mosangalala masiku ano.
a Ngati Mkhristu wachita chigololo, mwamuna kapena mkazi wake wosalakwayo ali ndi ufulu wosankha kumukhululukira kapena ayi.—Mateyu 19:9.
b Buku linanso limene uthenga wake kwenikweni sunkapita kwa Aisiraeli, ndi la Nahumu. Uthenga wa m’bukuli unkapita kwa anthu a ku Nineve.