Maliko
15 Mwamsanga m’bandakucha, ansembe aakulu, akulu ndi alembi, kutanthauza Khoti lonse Lalikulu la Ayuda,* anasonkhana pamodzi ndi kugwirizana chimodzi.+ Kenako anamanga Yesu ndi kukam’pereka kwa Pilato.+ 2 Choncho Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu+ ya Ayuda?” Iye anayankha kuti: “Mukunena nokha.”+ 3 Koma ansembe aakulu anapitiriza kumuneneza zinthu zambiri.+ 4 Tsopano Pilato anamufunsanso kuti: “Kodi ukusowa choyankha?+ Taona kuchuluka kwa milandu imene akukuneneza.”+ 5 Koma Yesu sanayankhenso chilichonse, moti Pilato anadabwa kwambiri.+
6 Pa chikondwerero chilichonse, Pilato anali kumasulira anthu mkaidi mmodzi amene iwo apempha.+ 7 Pa nthawiyo panali wina wotchedwa Baraba, amene anali m’ndende limodzi ndi oukira boma. Iwo anapha munthu pa kuukira kwawoko.+ 8 Choncho khamu la anthu linafika ndi kuyamba kupempha malinga ndi zimene iye anali kuwachitira nthawi zonse. 9 Pilato anawafunsa kuti: “Kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?”+ 10 Pakuti iye anadziwa kuti ansembe aakulu anamupereka chifukwa cha kaduka.+ 11 Koma ansembe aakulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba.+ 12 Poyankha, Pilato anawafunsa kuti: “Nanga uyu amene mumati ndi mfumu+ ya Ayuda, ndichite naye chiyani?”+ 13 Pamenepo iwo anafuula kuti: “M’pachikeni!”+ 14 Koma Pilato anapitiriza kuwafunsa kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma atatero m’pamene anawonjezera kufuula kuti: “M’pachikeni!”+ 15 Pamenepo Pilato, pofuna kukwaniritsa zofuna za anthuwo,+ anawamasulira Baraba. Ndipo atalamula kuti Yesu amukwapule, anamupereka kuti akamupachike.+
16 Tsopano asilikali anamutenga ndi kupita naye m’bwalo lamkati kunyumba ya bwanamkubwa. Kumeneko anasonkhanitsa khamu lonse la asilikali.+ 17 Ndiyeno anamuveka chovala cha maonekedwe ofiirira ndi kuluka chisoti chachifumu chaminga ndi kumuveka.+ 18 Tsopano anayamba kum’lonjera kuti: “Mtendere ukhale nanu,+ inu Mfumu ya Ayuda!” 19 Komanso anali kum’menya m’mutu ndi bango ndi kumulavulira, ndipo anali kugwada ndi kumuweramira.+ 20 Atamaliza kumuchitira zachipongwezo, anamuvula chovala chofiirira chija ndi kumuveka malaya ake akunja. Atatero anatuluka naye kupita kokamupachika.+ 21 Komanso, iwo anasenzetsa mtengo wake wozunzikirapo* munthu wongodutsa, dzina lake Simoni wa ku Kurene, amene anali kuchokera kudera la kumidzi, bambo wa Alekizanda ndi Rufu.+
22 Choncho anafika naye kumalo otchedwa Gologota. Liwuli akalimasulira, limatanthauza Malo a Chibade.+ 23 Kumeneko anayesa kum’patsa vinyo wosakaniza ndi mule,+ koma iye anakana.+ 24 Pamenepo anamupachika pamtengo ndi kugawana malaya ake akunja+ mwa kuchita maere pamalayawo, kuti aone chimene munthu aliyense angatenge.+ 25 Tsopano nthawi ili cha m’ma 9 koloko m’mawa,*+ iwo anam’pachika. 26 Ndiyeno mawu osonyeza mlandu wake+ anawalemba pamwamba pake kuti: “Mfumu ya Ayuda.”+ 27 Komanso iwo anapachika achifwamba awiri limodzi ndi iye. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.+ 28* —— 29 Anthu amene anali kudutsa pamenepo anali kumulankhula monyoza.+ Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: “Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu,+ 30 dzipulumutse. Tsika pamtengo wozunzikirapowo.”+ 31 Chimodzimodzinso ansembe aakulu. Nawonso anali kumuchita chipongwe limodzi ndi alembi. Iwo anali kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikum’kanika!+ 32 Tsopanotu Khristu, Mfumu ya Isiraeli, itsike pamtengo wozunzikirapowo, kuti ife tione ndi kukhulupirira.”+ Ngakhale amene anapachikidwa naye limodziwo analinso kumunyoza.+
33 Nthawi itafika cha m’ma 12 koloko masana,* kunagwa mdima m’dziko lonselo mpaka 3 koloko masana.*+ 34 Ndipo cha m’ma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 35 Tsopano ena mwa anthu amene anaimirira chapafupi, atamva zimenezo, anayamba kunena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.”+ 36 Koma wina anathamanga kukaviika chinkhupule m’vinyo wowawasa, kenako anachiika kubango ndi kum’patsa kuti amwe,+ ndikunena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”+ 37 Ndiyeno Yesu anafuula mokweza mawu, ndipo anatsirizika.+ 38 Pamenepo nsalu yotchinga+ ya m’nyumba yopatulika inang’ambika pakati, kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 39 Tsopano, kapitawo wa asilikali amene anaimirira chapafupi moyang’ana Yesu, ataona zimene zinachitika pa nthawi imene anatsirizika, ananena kuti: “Ndithudi munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+
40 Panali amayi amene anali kuonerera chapatali ndithu,+ ena mwa iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo Wamng’ono ndi Yose, komanso Salome,+ 41 amene anali kuyenda naye limodzi+ ndi kumutumikira pamene anali ku Galileya. Panalinso amayi ena ambiri amene anabwera naye limodzi kuchokera ku Yerusalemu.+
42 Tsopano madzulo, popeza linali Tsiku Lokonzekera, kapena kuti tsiku loti m’mawa mwake ndi sabata, 43 Yosefe wa ku Arimateya, munthu wodziwika wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda, amenenso anali kuyembekezera ufumu wa Mulungu,+ anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo+ wa Yesu. 44 Koma Pilato anali kukayikira ngati anali atamwalira kale, choncho anaitanitsa kapitawo wa asilikali ndi kumufunsa ngatidi iye wamwalira kale. 45 Atatsimikizira kuchokera kwa kapitawo wa asilikaliyo, analola kuti Yosefe akatenge mtembowo.+ 46 Ndiyeno Yosefe anagula nsalu yabwino kwambiri ndi kumutsitsa. Atatero anamukulunga ndi nsalu yabwino kwambiri ija ndi kumuika+ m’manda+ amene anawasema m’thanthwe. Anagubuduza chimwala ndi kutseka pakhomo la manda achikumbutsowo.+ 47 Koma Mariya Mmagadala ndi Mariya mayi wa Yose, anali kuyang’anitsitsa pamene anaikidwapo.+