2 Yohane
1 Ine monga mkulu,+ ndikulembera mayi wosankhidwa+ ndi Mulungu ndiponso ana ake amene ndimawakondadi.+ Ndipo si ine ndekha amene ndimawakonda. Onse amene adziwa choonadi amawakondanso.+ 2 Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chili mumtima mwathu,+ ndipo chidzakhalabe ndi ife mpaka muyaya.+ 3 Tidzalandira kukoma mtima kwakukulu,+ chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate+ wathu ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, limodzi ndi choonadi ndiponso chikondi.+
4 Ndikusangalala kwambiri kuti ndapeza ena mwa ana+ anu akuyenda m’choonadi,+ mogwirizana ndi lamulo limene tinalandira kwa Atate.+ 5 Chotero ndikukupemphani mayi, kuti tonse tizikondana.+ Sindikukulemberani zimenezi ngati munthu amene ndikukupatsani lamulo latsopano,+ koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pachiyambi.+ 6 Ndipo chikondi chimenechi chimatanthauza kuti+ tiziyendabe motsatira malamulo ake.+ Monga mmene munamvera kuyambira pachiyambi, lamulo lake ndi lakuti mupitirize kuyenda m’chikondi,+ 7 popeza anthu onyenga ambiri alowa m’dziko,+ amene amatsutsa zakuti kalero Yesu Khristu anabwera monga munthu.+ Amene amachita zimenezi ndi wonyenga+ uja ndiponso wokana Khristu.+
8 Samalani kuti musalephere kulandira mphoto ya zinthu zimene tazigwirira kale ntchito, kuti mudzalandire mphoto yokwanira.+ 9 Aliyense amene amachita zosemphana ndi zimene Khristu amaphunzitsa,+ ndiye kuti akukana Mulungu.+ Koma amene amachita zinthu mogwirizana ndi zimene iye amaphunzitsa, amavomerezedwa ndi Atate ndiponso Mwana.+ 10 Wina akabwera kwa inu ndi chiphunzitso chosiyana ndi ichi, musamulandire m’nyumba zanu+ kapena kumupatsa moni.+ 11 Aliyense amene wamupatsa moni akugawana naye ntchito zake zoipazo.+
12 Ngakhale kuti ndili ndi zambiri zoti ndikulembereni, sindikufuna kuzilemba papepala ndi inki,+ koma ndikuyembekezera kubwera kwa inu kuti ndidzalankhule nanu pamasom’pamaso,+ kuti mudzakhale ndi chimwemwe+ chokwanira.+
13 Ana a m’bale wanu wosankhidwa ndi Mulungu, akupereka moni.+