Zekariya
13 “Pa tsiku limenelo, a mʼnyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu adzawakumbira chitsime kuti ayeretsedwe ku machimo awo.”+
2 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzafufuta mayina a mafano mʼdziko lonseli+ ndipo sadzakumbukiridwanso. Ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa. 3 Munthu aliyense akadzayamba kulosera, bambo ake ndi mayi ake amene anamubereka adzamuuza kuti, ‘Iwe ufa ndithu, chifukwa walankhula zonama mʼdzina la Yehova.’ Ndiyeno bambo ndi mayi akewo adzamulasa chifukwa choti akulosera.+
4 Pa tsikulo, mneneri aliyense azidzachita manyazi ndi masomphenya ake pamene akulosera. Sadzavalanso chovala chapadera chaubweya+ kuti anamize anthu. 5 Ndipo azidzanena kuti, ‘Ine siine mneneri. Ndine mlimi, chifukwa munthu wina anandigula ndili wamngʼono.’ 6 Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi mabala amene ali pakati pa mapewa akowa* watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Mabalawa anabwera chifukwa chomenyedwa kunyumba kwa anzanga.’”*
7 “Iwe lupanga, nyamuka ubaye mʼbusa wanga.+
Ubaye munthu yemwe ndi mnzanga,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
8 Yehova wanena kuti, “Mʼdziko lonseli,
Anthu awiri pa anthu atatu alionse adzaphedwa.
Ndipo wachitatuyo ndi amene adzatsale.”
9 “Ine ndidzatenga anthu otsalawo nʼkuwaika pamoto.
Ndipo ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva
Komanso kuwayesa ngati mmene amayesera golide.+
Iwo adzaitana dzina langa,
Ndipo ine ndidzawayankha.
Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+
Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”