Numeri
17 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo utenge ndodo imodzi kuchokera ku fuko lililonse, kwa mtsogoleri wa fukolo.+ Zikhalepo ndodo 12 ndipo ulembe dzina la mtsogoleri aliyense pa ndodo yake. 3 Pandodo ya fuko la Levi ulembepo dzina la Aroni, chifukwa ndodo iliyonse ikuimira mtsogoleri wa fuko. 4 Ndodozo uziike mʼchihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+ 5 Ndodo ya munthu amene ndimusankheyo+ idzaphuka, ndipo ndidzathetsa kungʼungʼudza kwa Aisiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine+ komanso motsutsana ndi iwe.”+
6 Choncho Mose analankhula ndi Aisiraeli ndipo atsogoleri awo onse anapereka ndodo zawo. Mtsogoleri aliyense anapereka ndodo imodzi ya fuko lake. Panali ndodo 12, ndipo imodzi inali ya Aroni. 7 Ndiyeno Mose anakaika ndodozo pamaso pa Yehova mʼchihema cha Umboni.
8 Tsiku lotsatira, Mose atalowa mʼchihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni yoimira nyumba ya Levi yaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inkamasula maluwa komanso kubereka zipatso za amondi zakupsa. 9 Kenako Mose anatenga ndodo zonse pamaso pa Yehova nʼkupita nazo kwa Aisiraeli onse. Atsogoleri aja anayangʼana ndodozo, ndipo aliyense anatengapo yake.
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo ya Aroni+ patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana opandukawa,+ nʼcholinga chakuti asiye kungʼungʼudza motsutsana ndi ine komanso kuti asafe.” 11 Nthawi yomweyo Mose anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Anachitadi zomwezo.
12 Ndiyeno Aisiraeli anauza Mose kuti: “Tsopano ife tifa. Ndithudi titha ife. Tonse titha basi. 13 Aliyense amene ayerekeze kuyandikira chihema cha Yehova afa.+ Koma zoona ife tife mwa njira imeneyi?”+