Numeri
28 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti, ‘Muzionetsetsa kuti mukupereka kwa ine nsembe yanga, yomwe ndi chakudya changa. Pa nthawi yake yoikidwiratu muzipereka nsembe zanga zowotcha pamoto, kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa ine.’+
3 Uwauze kuti, ‘Nsembe yowotcha pamoto imene muzipereka kwa Yehova ndi iyi: tsiku lililonse muzipereka nsembe yopsereza ya ana a nkhosa awiri amphongo, achaka chimodzi komanso opanda chilema.+ 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+ 6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova kuti ikhale nsembe yakafungo kosangalatsa,* yowotcha pamoto. 7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa chokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense+ muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsa mʼmalo oyera. 8 Mwana wa nkhosa wamphongo winayo muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.* Muzimupereka limodzi ndi nsembe yambewu ndiponso yachakumwa, mofanana ndi nsembe ya mʼmamawa ija. Izikhala nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+
9 Koma pa tsiku la Sabata,+ muzipereka nsembe ana a nkhosa awiri amphongo opanda chilema. Muziwapereka pamodzi ndi ufa wosalala kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta, ndipo uzikhala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Muziperekanso nsembe yake yachakumwa. 10 Imeneyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata, ndipo muziipereka nthawi zonse limodzi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku komanso nsembe yake yachakumwa.+
11 Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse,* muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ 12 Pa ngʼombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wothira mafuta wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yake yambewu.+ Nkhosa yamphongo imodziyo muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta, wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yemwe ndi nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa,*+ nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 14 Pa nyama iliyonse yoperekedwa nsembe, muziperekanso nsembe yachakumwa. Ngʼombe yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo+ wokwana hafu ya muyezo wa hini. Nkhosa yamphongo+ muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo muzimupereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.+ Zinthu zimenezi muzizipereka monga nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi ndipo muzizipereka mwezi uliwonse pa chaka. 15 Muziperekanso mbuzi yaingʼono kuti ikhale nsembe yamachimo kwa Yehova, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.
16 Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14, pazikhala Pasika wa Yehova.+ 17 Ndiyeno pa tsiku la 15 la mwezi umenewu pazikhala chikondwerero. Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda zofufumitsa.+ 18 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli. 19 Muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova, yomwe ndi nsembe yowotcha pamoto. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazo nʼzopanda chilema.+ 20 Muzipereka nsembe zimenezi limodzi ndi nsembe zake zambewu. Ngʼombe yamphongo iliyonse muziipereka limodzi ndi ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Nkhosa yamphongoyo muziipereka limodzi ndi ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Ufawo uzikhala wothira mafuta.+ 21 Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense pa ana a nkhosa 7 amenewo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 22 Komanso muzipereka mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuti ikhale yophimbira machimo anu. 23 Muzipereka nsembe zimenezi, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yamʼmamawa ya tsiku ndi tsiku. 24 Muzipereka nsembe zimenezi mofanana tsiku lililonse kwa masiku 7. Muzizipereka monga chakudya, nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza ya nthawi zonse komanso nsembe yake yachakumwa. 25 Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli.+
26 Ndipo pa tsiku la zipatso zoyamba kucha,+ pamene muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova,+ paphwando lanu la masabata, muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli.+ 27 Muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo, achaka chimodzi.+ 28 Muziperekanso nsembe yake yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ngʼombe yamphongo iliyonse. Pa nkhosa yamphongo imodziyo, muzipereka ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 29 Pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo, muzipereka ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 30 Komanso muzipereka mbuzi yaingʼono yophimbira machimo anu.+ 31 Muzipereka zimenezi kuwonjezera pa nsembe yanu yopsereza ya nthawi zonse ndi nsembe yake yambewu. Muzionetsetsa kuti nyamazo nʼzopanda chilema+ ndipo muzipereka limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.’”