-
Levitiko 5:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera azilipira mwa kubweza zinthu zopatulikazo ndiponso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a malipirowo. Malipirowo aziwapereka kwa wansembe, ndipo mwa kupereka nkhosa ya nsembe ya kupalamula, wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo azikhululukidwa.+
-
-
1 Samueli 12:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ine ndaima pamaso panu. Munditsutse pamaso pa Yehova ndi pamaso pa wodzozedwa+ wake: Alipo kodi amene ndinam’tengerapo ng’ombe kapena bulu wake?+ Alipo kodi amene ndinam’chitirapo chinyengo, kapena kum’pondereza? Kodi ndinalandirapo chiphuphu kwa aliyense kuti ndisaone zimene anachita?+ Ndili wokonzeka kukubwezerani anthu inu.”+
-