43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ m’chipululu cha dera lokwererapo, wothawirako Arubeni, mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, wothawirako Agadi, ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, wothawirako Amanase.+
8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.
3 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda m’manja mwa mfumu ya Siriya.”
80 Kuchokera ku fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto,