-
Oweruza 18:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Choncho amuna asanu aja anapitiriza ulendo wawo ndipo anafika kumzinda wa Laisi.+ Kumeneko anaona kuti anthu a mumzindawo anali kukhala mosadalira aliyense, malinga ndi chikhalidwe cha Asidoni. Iwo anali kukhala phee, mosatekeseka,+ ndipo panalibe amene anawagonjetsa n’kumawachitira nkhanza kapena kuwavutitsa m’dzikolo. Kuwonjezera apo, anali kukhala kutali kwambiri ndi Asidoni+ ndipo sanali kuyenderana ndi anthu a m’madera ena.
-