Oweruza 13:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Pamenepo Manowa anayamba kuchonderera Yehova kuti: “Yehova,+ lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize+ zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”+ Oweruza 13:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Mulungu woona anamvetsera mawu a Manowa,+ moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anam’peza atakhala pansi kunja kwa mzinda. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa. Oweruza 13:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Pamenepo Manowa anadziwa kuti anali mngelo wa Yehova.+ Aheberi 13:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+
8 Pamenepo Manowa anayamba kuchonderera Yehova kuti: “Yehova,+ lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwerenso kuti adzatilangize+ zoyenera kuchita ndi mwana amene adzabadweyo.”+
9 Mulungu woona anamvetsera mawu a Manowa,+ moti mngelo wa Mulungu woona uja anabweranso kwa mkaziyo, ndipo anam’peza atakhala pansi kunja kwa mzinda. Pa nthawiyi sanali limodzi ndi mwamuna wake Manowa.
21 Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Pamenepo Manowa anadziwa kuti anali mngelo wa Yehova.+