7 Koma iye wandiuza kuti, ‘Pakuti udzakhala ndi pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.+ Choncho, usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo usadye chilichonse chodetsedwa, chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri wa Mulungu potuluka m’mimba mpaka pa tsiku la imfa yake.’”+