-
Numeri 4:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Aroni ndi ana ake akamaliza kuphimba zinthu za m’malo oyera+ ndi ziwiya zonse+ za m’malo oyerawo posamutsa msasa, ana a Kohati azilowamo n’kudzazinyamula.+ Iwo asamakhudze+ zinthu za m’malo oyerazo chifukwa angafe. Zinthu zimenezi ndizo katundu wa m’chihema chokumanako amene ana a Kohati azinyamula.+
-