12 Ndipo Alevi+ oimba a m’gulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni,+ ana awo ndi abale awo, onsewa atavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe+ ndi azeze,+ anaimirira kum’mawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwanira 120 oimba malipenga.+