12 Alevi onse oimba+ a mʼgulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni+ ndiponso ana awo ndi abale awo, anavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze ndipo anaimirira kumʼmawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwana 120 oimba malipenga.+