11 Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa.+ Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake,+ ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.+ Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.+
12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mmene amachitira munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa+ zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika.+ Pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani, ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.+