Yesaya
40 “Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,” akutero Mulungu wanu anthu inu.+ 2 “Mulankhuleni Yerusalemu momufika pamtima.+ Muuzeni mofuula kuti ntchito yake yogwira mokakamizidwa yatha,+ ndiponso kuti zolakwa zake zalipiridwa.+ Pakuti kuchokera m’dzanja la Yehova, iye walandira malipiro okwanira a machimo ake onse.”+
3 Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti:+ “Konzani njira ya Yehova+ anthu inu! Wongolani msewu wa Mulungu wathu wodutsa m’chipululu.+ 4 Chigwa chilichonse chikwezedwe m’mwamba,+ ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zitsitsidwe.+ Malo okumbikakumbika asalazidwe ndipo malo azitundazitunda akhale chigwa.+ 5 Ulemerero wa Yehova ndithu udzaonekera+ ndipo anthu onse adzauonera limodzi,+ pakuti pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.”+
6 Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lankhula mofuula!”+ Ndiye wina akuti: “Ndilankhule mofuula za chiyani?”
“Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira ndipo kukoma mtima kwawo konse kosatha kuli ngati maluwa akutchire.+ 7 Udzu wobiriwirawo wauma ndipo maluwawo afota+ chifukwa mpweya wa Yehova wauzirapo.+ Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.+ 8 Udzu wobiriwirawo wauma. Maluwawo afota.+ Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”+
9 Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Ziyoni,+ kwera phiri lalitali.+ Lankhula mwamphamvu ndiponso mofuula, iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.+ Fuula! Usachite mantha.+ Uza mizinda ya ku Yuda kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu.”+ 10 Taonani! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabwera ngati wamphamvu ndipo dzanja lake lizidzalamulira m’malo mwa iyeyo.+ Mphoto yake ili ndi iyeyo+ ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.+ 11 Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa.+ Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake,+ ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.+ Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.+
12 Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo? 13 Ndani anayezapo mzimu wa Yehova? Ndi munthu uti amene angamupatse malangizo kapena kumuphunzitsa kanthu?+ 14 Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsetsa zinthu? Ndani amamuphunzitsa njira ya chilungamo? Ndani amamuphunzitsa kuti azidziwa zinthu,+ ndipo ndani amamuphunzitsa kuti akhale womvetsa bwino zinthu?+
15 Taonani! Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.+ Iyetu amanyamula zilumba+ ngati kuti ndi fumbi. 16 Ngakhale mitengo yonse ya ku Lebanoni singakwane kusonkhezera moto kuti usazime, ndipo nyama zake zam’tchire+ si zokwanira kukhala nsembe yopsereza.+ 17 Mitundu yonse ndi yopanda pake pamaso pake.+ Amaiona ngati si kanthu n’komwe, ngati kuti iyo kulibe.+
18 Kodi anthu inu Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani,+ ndipo kodi mungapange chiyani choti mumufanizire nacho?+ 19 Mmisiri wapanga chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Mmisiri wina wa zitsulo wachikuta ndi golide,+ ndipo akuchipangira matcheni asiliva.+ 20 Munthu amasankha mtengo wosawola kuti ukhale ngati chopereka.+ Amafunafuna mmisiri waluso kuti amupangire chifaniziro chosema+ chimene sichingagwedezeke.+
21 Kodi anthu inu simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi simunauzidwe kuyambira pa chiyambi? Kodi simunamvetsetse umboni umene wakhalapo kuyambira pamene dziko lapansi linakhalapo?+ 22 Pali Winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira,+ limene okhalamo ake ali ngati ziwala. Iye anayala kumwamba ngati nsalu yopyapyala, ndipo anakutambasula ngati hema wokhalamo.+ 23 Iye amatsitsa anthu olemekezeka, ndipo amachititsa oweruza a padziko lapansi kuoneka ngati sanakhalepo n’komwe.+
24 Iwo sanabzalidwe n’komwe ndipo sanafesedwe. Chitsa chawo sichinazike mizu munthaka.+ Munthu akhoza kungowauzira iwo n’kuuma,+ ndipo mphepo yamkuntho idzawauluza ngati mapesi.+
25 “Koma kodi anthu inu mungandiyerekezere ndi ndani kuti ndifanane naye?” akutero Woyerayo.+ 26 “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?+ Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake.+ Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa,+ ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa.
27 “N’chifukwa chiyani iwe Yakobo, iwe Isiraeli, ukunena kuti: ‘Njira yanga yabisika kwa Yehova,+ ndipo zoti anthu sakundichitira chilungamo Mulungu wanga sakuziona’?+ 28 Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+ 29 Iye amapereka mphamvu kwa munthu wotopa,+ ndipo wofooka amam’patsa nyonga zochuluka.+ 30 Anyamata adzatopa n’kufooka ndipo amuna achinyamata adzapunthwa, 31 koma anthu odalira+ Yehova adzapezanso mphamvu.+ Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Adzathamanga koma osafooka. Adzayenda koma osatopa.”+