7 iye wapatulanso tsiku lina chifukwa wagwiritsa ntchito mawu akuti “Lero” mu salimo la Davide, pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri. Izi zikugwirizana ndi zimene tanena kale zija kuti: “Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+ musaumitse mitima yanu.”+