8 Ine ndikuwabweretsa kuchokera kudziko la kumpoto,+ ndipo ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Pakati pawo padzakhala anthu akhungu, olumala, akazi apakati komanso akazi amene atsala pang’ono kubereka.+ Adzabwerera kumalo ano ali mpingo waukulu.+