3 Pakuti nthawi+ imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli+ pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira,+ zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo,+ maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.+