30 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupatse aliyense malinga ndi njira zake zonse,+ popeza mukudziwa mtima wake+ (popeza inu nokha ndiye mumadziwa bwino mtima wa ana a anthu).+
10 Ine Yehova ndimafufuza mtima+ ndi kusanthula impso.+ Munthu aliyense ndimamuchitira zinthu monga mwa zochita zake,+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+