Salimo 88:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.] Salimo 115:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Akufa satamanda Ya,+Ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.+ Salimo 146:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+ Yesaya 38:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pakuti Manda sangakutamandeni.+ Imfa singakulemekezeni.+Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kukhulupirika kwanu.+ Yohane 11:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Atanena zimenezi, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”+
10 Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.]
4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+
18 Pakuti Manda sangakutamandeni.+ Imfa singakulemekezeni.+Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kukhulupirika kwanu.+
11 Atanena zimenezi, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.”+