Miyambo 28:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+ Yesaya 1:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+ Yeremiya 5:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Nyumba zawo zadzaza chinyengo+ ngati mmene mbalame zimadzazira m’chikwere.* N’chifukwa chake iwo alemera ndipo apeza chuma chambiri.+ Yakobo 5:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.
20 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri,+ koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+
27 Nyumba zawo zadzaza chinyengo+ ngati mmene mbalame zimadzazira m’chikwere.* N’chifukwa chake iwo alemera ndipo apeza chuma chambiri.+
4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.