-
Ezekieli 3:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Munthu wolungama akasiya chilungamo chake+ n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ine n’kumuikira chopunthwitsa pamaso pake,+ iyeyo adzafa chifukwa chakuti sunamuchenjeze. Adzafa chifukwa cha tchimo lake+ ndipo zinthu zolungama zimene anachita sizidzakumbukiridwa,+ koma magazi ake ndidzawafuna kwa iweyo.+
-
-
Ezekieli 18:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 “‘Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo,+ akamachita zopanda chilungamo+ n’kumakhalabe ndi moyo, zinthu zolungama zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa.+ Iye adzafa chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika ndiponso chifukwa cha machimo ake amene anachita.+
-