Yeremiya 17:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.+ Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi m’mitima+ yawo ndi panyanga za guwa lansembe.+ Hoseya 8:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Iwo anali kupereka nsembe zanyama ngati mphatso kwa ine+ ndipo anali kuzidya, koma ine Yehova sindinakondwere nazo.+ Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo. Ndidzawaimba mlandu chifukwa cha machimo awo+ ndiponso chifukwa chakuti iwo anabwerera ku Iguputo.+ Nahumu 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+ komatu Yehova salephera kulanga wolakwa.+ Njira yake ili mumphepo yowononga ndi mumphepo yamkuntho. Mitambo ndilo fumbi lopondapo mapazi ake.+
17 “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.+ Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi m’mitima+ yawo ndi panyanga za guwa lansembe.+
13 Iwo anali kupereka nsembe zanyama ngati mphatso kwa ine+ ndipo anali kuzidya, koma ine Yehova sindinakondwere nazo.+ Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo. Ndidzawaimba mlandu chifukwa cha machimo awo+ ndiponso chifukwa chakuti iwo anabwerera ku Iguputo.+
3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+ komatu Yehova salephera kulanga wolakwa.+ Njira yake ili mumphepo yowononga ndi mumphepo yamkuntho. Mitambo ndilo fumbi lopondapo mapazi ake.+