Yesaya 53:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+ 1 Akorinto 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ndinakupatsirani zija, zimenenso ineyo ndinalandira,+ panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba.+ Aheberi 9:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo? 1 Petulo 2:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 1 Yohane 3:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Inu mukudziwanso kuti iye anaonekera kuti achotse machimo athu,+ ndipo mwa iye mulibe tchimo.+
11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+
3 Mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ndinakupatsirani zija, zimenenso ineyo ndinalandira,+ panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba.+
14 kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo?
24 Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+