23 Chotero, Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu mpaka nyama, zokwawa pansi mpaka zolengedwa zouluka m’mlengalenga, anazisesa zonse padziko lapansi.+ Koma Nowa yekha, pamodzi ndi amene anali naye limodzi m’chingalawacho, anapulumuka.+