Genesis 3:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+ Salimo 146:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+ Mlaliki 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse+ komanso salandira mphoto iliyonse,* chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zimaiwalika.+ Mlaliki 9:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda*+ kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru. Ezekieli 18:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe.* Aroma 5:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa.+ Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa . . .+ 1 Akorinto 15:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Monga zilili kuti anthu onse amafa chifukwa cha Adamu,+ anthu onse adzapatsidwanso moyo kudzera mwa Khristu.+
19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+
4 Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+
5 Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse+ komanso salandira mphoto iliyonse,* chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zimaiwalika.+
10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda*+ kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru.
4 Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe.*
12 Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa.+ Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa . . .+
22 Monga zilili kuti anthu onse amafa chifukwa cha Adamu,+ anthu onse adzapatsidwanso moyo kudzera mwa Khristu.+