Genesis 26:34, 35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Muhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Muhiti.+ 35 Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+ Genesis 27:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Izi zitachitika, Rabeka ankauza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo chifukwa cha akazi a Chihetiwa.+ Ngati Yakobo nayenso angatenge mkazi pakati pa akazi a Chiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+
34 Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Muhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Muhiti.+ 35 Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+
46 Izi zitachitika, Rabeka ankauza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo chifukwa cha akazi a Chihetiwa.+ Ngati Yakobo nayenso angatenge mkazi pakati pa akazi a Chiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+