8 Koma Mulungu anawapulumutsa kuti dzina lake lilemekezedwe,+
Kuti mphamvu zake zidziwike.+
9 Iye analamula ndipo Nyanja Yofiira inauma.
Anatsogolera anthu ake kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akudutsa mʼchipululu.+
10 Anawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankadana nawo+
Ndipo anawawombola mʼmanja mwa mdani.+
11 Madzi anamiza adani awo,
Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+