-
Aheberi 9:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Chifukwa panamangidwa chipinda choyamba cha chihema ndipo mʼchipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo ndi mikate yoonetsa kwa Mulungu,*+ ndipo chinkatchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+ 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe+ ndi likasa la pangano+ lokutidwa ndi golide.+ Mulikasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana,+ ndodo ya Aroni imene inaphuka ija+ komanso miyala yosema+ ya pangano.
-