-
Levitiko 24:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 3 Aroni azikhazika nyale kunja kwa katani ya Malo Oyera Koposa mʼchihema chokumanako. Nyalezo ziziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka mʼmawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse.
-
-
1 Mafumu 7:48, 49Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
48 Solomo anapanga zinthu zonse zapanyumba ya Yehova. Anapanga guwa lansembe+ lagolide komanso tebulo yagolide+ yoikapo mkate wachionetsero. 49 Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino ndipo anaziika pafupi ndi chipinda chamkati, anaika 5 kumanja, 5 kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa agolide,+ nyale zagolide, zopanira zagolide zozimitsira nyale,+
-