Ekisodo 32:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Pa tsiku lotsatira, Mose anauza anthuwo kuti: “Mwachita tchimo lalikulu kwambiri. Choncho ndipita kuphiri kwa Yehova kuti mwina ndingakamuchonderere kuti akukhululukireni tchimo lanu.”+ Levitiko 16:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mʼchihema chokumanako musamapezeke munthu wina aliyense kuyambira nthawi imene Aroni walowa mʼmalo oyera kukaphimba machimo mpaka kutulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake, a banja lake+ ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+ Numeri 15:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Wansembe azikapereka nsembe yophimba machimo a gulu lonse la Aisiraeli. Akatero, anthuwo adzakhululukidwa+ chifukwa analakwitsa mosazindikira, komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova ndiponso apereka nsembe yamachimo kwa Yehova chifukwa cha zimene analakwitsazo. Aefeso 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kudzera mwa mwana wakeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake,+ inde, takhululukidwa machimo athu,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kwakukulu. Aheberi 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu.
30 Pa tsiku lotsatira, Mose anauza anthuwo kuti: “Mwachita tchimo lalikulu kwambiri. Choncho ndipita kuphiri kwa Yehova kuti mwina ndingakamuchonderere kuti akukhululukireni tchimo lanu.”+
17 Mʼchihema chokumanako musamapezeke munthu wina aliyense kuyambira nthawi imene Aroni walowa mʼmalo oyera kukaphimba machimo mpaka kutulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake, a banja lake+ ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+
25 Wansembe azikapereka nsembe yophimba machimo a gulu lonse la Aisiraeli. Akatero, anthuwo adzakhululukidwa+ chifukwa analakwitsa mosazindikira, komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova ndiponso apereka nsembe yamachimo kwa Yehova chifukwa cha zimene analakwitsazo.
7 Kudzera mwa mwana wakeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake,+ inde, takhululukidwa machimo athu,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.
17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu.