-
Deuteronomo 29:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Mʼbadwo wa mʼtsogolo wa ana anu ndiponso mlendo wochokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi matenda amene Yehova wabweretsa mʼdzikoli—* 23 akadzaona kuti dziko lonse lawonongedwa ndi sulufule, mchere ndi kutentha, moti mʼdzikomo simungadzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, ndipo likuoneka ngati Sodomu ndi Gomora,+ Adima ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga ndi ukali komanso mkwiyo wake—* 24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’
-
-
Ezekieli 5:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Udzakhala chinthu chimene anthu azidzachinyoza komanso kuchichitira chipongwe.+ Zimene zidzakuchitikire zidzakhala chenjezo ndipo zidzabweretsa mantha kwa anthu a mitundu yokuzungulira. Zimenezi zidzachitika ndikadzapereka chiweruzo kwa iwe komanso kukulanga mokwiya ndiponso mwaukali. Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.
-