-
Deuteronomo 9:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa mʼdziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba,*+ 2 yokhalanso ndi anthu amphamvu ndi aatali, ana a Anaki,+ amene inu mukuwadziwa ndipo munamva anthu akunena za iwo kuti, ‘Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?’
-