48 Koma amene sanadziwe ndipo wachita zinthu zofunika kumʼkwapula, adzamukwapula zikoti zochepa. Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye. Ndipo aliyense amene anaikidwa kuti aziyangʼanira zinthu zochuluka, anthu adzafunanso zochuluka kwa iye.+