-
Oweruza 6:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka 7.+ 2 Amidiyaniwo anayamba kupondereza Aisiraeli.+ Chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli anakonza malo oti azibisalako* mʼmapiri, mʼmapanga ndi mʼmalo ena ovuta kufikako.+ 3 Aisiraeli akalima minda yawo, Amidiyani, Aamaleki+ ndi anthu a Kumʼmawa+ ankabwera kudzawaukira. 4 Ankabwera nʼkuwawonongera zokolola zawo zonse mpaka kukafika ku Gaza. Sankawasiyira chakudya chilichonse ngakhalenso nkhosa, ngʼombe kapena bulu.+ 5 Iwo ankabwera ndi ziweto zawo ndi matenti awo. Ankabwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Ankabwera mʼdzikomo nʼkumaliwononga.
-