-
Numeri 32:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mose anawauza kuti: “Chabwino, koma zitheka ngati mutachita izi: Mutenge zida nʼkukamenya nkhondo pamaso pa Yehova.+ 21 Komanso ngati aliyense wa inu atatenga zida zake zankhondo nʼkuwoloka Yorodano pamaso pa Yehova, mpaka atathamangitsa adani ake pamaso pake,+ 22 ndiponso mpaka dzikolo litagonjetsedwa pamaso pa Yehova.+ Pambuyo pake mukhoza kudzabwerera+ ndipo mudzakhala opanda mlandu kwa Yehova ndi kwa Isiraeli. Kenako dzikoli lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.+
-
-
Yoswa 22:1-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Kenako Yoswa anaitana anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, 2 nʼkuwauza kuti: “Mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani,+ ndiponso mwamvera zonse zimene ine ndinakulamulani.+ 3 Simunawasiye abale anu nthawi yonseyi mpaka lero+ ndipo mwasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu.+ 4 Panopa Yehova Mulungu wanu wapatsa abale anu mpumulo mogwirizana ndi zimene anawalonjeza.+ Choncho bwererani, mupite kumatenti anu kudera limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, kutsidya lina* la Yorodano.+
-