-
Numeri 21:21-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Tsopano Aisiraeli anatuma anthu kuti apite kwa Sihoni mfumu ya Aamori kukanena kuti:+ 22 “Tiloleni tidutse mʼdziko lanu. Sitikhotera mʼmunda uliwonse kapena mʼmunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu mpaka titadutsa mʼdziko lanu.”+ 23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lake. Mʼmalomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkupita kukamenyana ndi Aisiraeli mʼchipululumo. Anakafika ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 24 Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ nʼkuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi Aamoni, chifukwa Yazeri+ anachita malire ndi Aamoni.+
-
-
Deuteronomo 2:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenya nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33 Yehova Mulungu wathu anamupereka kwa ife ndipo tinamugonjetsa limodzi ndi ana ake komanso anthu ake onse. 34 Pa nthawi imeneyo, tinalanda mizinda yake yonse ndi kuwononga mzinda wina uliwonse. Tinapha amuna, akazi ndi ana ndipo sitinasiye munthu aliyense ndi moyo.+
-