-
Yoswa 13:2-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Madera amene atsala ndi awa:+ Madera onse a Afilisiti ndi madera onse a Agesuri.+ 3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo* kumʼmawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi, lomwe linkaonedwa kuti ndi la Akanani.)+ Komanso madera a olamulira 5 a Afilisiti+ omwe ndi Gaza, Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ ndiponso dera la Aavimu.+ 4 Kumʼmwera kwatsala dera lonse la Akanani. Patsalanso mzinda wa Asidoni+ wotchedwa Meara, mpaka kukafika ku Afeki kumalire a Aamori, 5 dera la Agebala+ ndiponso dera lonse la Lebanoni chakumʼmawa, kuyambira ku Baala-gadi mʼmunsi mwa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo-hamati.*+ 6 Ine ndidzathamangitsa pamaso pa Aisiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu+ komanso Asidoni+ onse. Iweyo ungopereka maderawa kwa Aisiraeli+ kuti akhale cholowa chawo mogwirizana ndi zimene ndinakulamula.+
-