-
Oweruza 13:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Kenako Manowa anatenga kamwana ka mbuzi ndi nsembe yambewu nʼkuzipereka nsembe kwa Yehova pathanthwe. Pamene ankachita zimenezi, Mulungu ankachita zodabwitsa Manowa ndi mkazi wake akuona. 20 Pamene malawi a moto ankakwera mʼmwamba kuchokera paguwa lansembelo, mngelo wa Yehova nayenso anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuona. Nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.
-