-
Numeri 15:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Koma ngati mukupereka ngʼombe yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapenanso kuti ikhale nsembe yamgwirizano kwa Yehova,+ 9 munthu amene akuperekayo azikapereka ngʼombe yamphongoyo limodzi ndi nsembe yambewu.+ Nsembe yambewuyo izikakhala yokwana magawo atatu a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo azikauthira mafuta okwana hafu ya muyezo wa hini. 10 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa.+ Vinyoyo azikakhala wokwana hafu ya muyezo wa hini. Akakhale nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
-