-
Aheberi 11:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Kodi ndiperekenso zitsanzo zina? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni,+ Baraki,+ Samisoni,+ Yefita,+ Davide+ komanso Samueli+ ndi aneneri ena. 33 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pankhondo,+ anachita chilungamo, analonjezedwa zinthu zina+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+ 34 Sanapse ndi moto,+ sanaphedwe ndi lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ anamenya nkhondo mwamphamvu+ ndiponso anathamangitsa magulu ankhondo.+
-