13 Kenako Yehova anayamba kugunda ngati mabingu ali kumwamba.+
Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke,+
Ndipo kunagwa matalala ndi makala a moto.
14 Anaponya mivi yake nʼkuwabalalitsa.+
Anaponya mphezi zake nʼkuwachititsa kuti asokonezeke.+
15 Pansi pa mitsinje panayamba kuonekera.+
Maziko a dziko lapansi anayamba kuonekera chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova,
Komanso chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu.+
16 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba,
Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+