-
2 Mbiri 2:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndipo inu mbuye wanga tumizani tirigu, balere, mafuta ndi vinyo zimene mwatilonjeza ife akapolo anu.+ 16 Ife tidula mitengo yambiri mmene inu mukufunira kuchokera ku Lebanoni,+ ndipo tiziimanga mʼmaphaka oti aziyandama nʼkuitumiza panyanja kukafika ku Yopa.+ Inu muzikaitengera kumeneko nʼkupita nayo ku Yerusalemu.”+
-
-
Ezara 3:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako anthuwo anapereka ndalama kwa anthu osema miyala+ ndi amisiri.+ Anaperekanso chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Turo chifukwa anabweretsa matabwa a mkungudza kudzera panyanja kuchokera ku Lebanoni kukafika ku Yopa.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi chilolezo chimene Koresi mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.+
-