-
2 Mbiri 9:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kuwonjezera pamenepo, atumiki a Hiramu ndi atumiki a Solomo amene anabwera ndi golide kuchokera ku Ofiri,+ anabweretsanso matabwa a mtengo wa mʼbawa ndi miyala yamtengo wapatali.+ 11 Mfumuyo inagwiritsa ntchito matabwa a mʼbawawo popanga masitepe a nyumba ya Yehova+ komanso a nyumba ya mfumu.+ Inagwiritsanso ntchito matabwawo kupanga azeze ndi zoimbira za zingwe za oimba.+ Matabwa a mʼbawa otere, sanaonekeponso mʼdziko la Yuda.
-