-
1 Mafumu 2:31-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Mfumuyo inamuuza kuti: “Chita zimene wakuuzazo. Ukamuphe nʼkumuika mʼmanda ndipo undichotsere ineyo komanso nyumba ya bambo anga magazi amene Yowabu anakhetsa popanda chifukwa.+ 32 Yehova adzachititsa kuti magazi ake akhale pamutu pake, chifukwa anapha ndi lupanga anthu awiri olungama komanso abwino kuposa iyeyo. Anachita zimenezi Davide bambo anga osadziwa. Iye anapha Abineri+ mwana wa Nera mkulu wa asilikali a Isiraeli+ ndiponso Amasa+ mwana wa Yeteri mkulu wa asilikali a Yuda.+ 33 Magazi awo adzakhala pamutu pa Yowabu ndi pamutu pa mbadwa zake mpaka kalekale.+ Koma mtendere wochokera kwa Yehova ukhale kwa Davide, mbadwa zake, nyumba yake ndiponso mpando wake wachifumu mpaka kalekale.” 34 Kenako Benaya mwana wa Yehoyada anapita kuchihemako nʼkukapha Yowabu ndipo anaikidwa mʼmanda kunyumba kwake mʼchipululu.
-