-
2 Mafumu 9:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Kenako Yehu anauza Bidikara msilikali wake womuthandiza, kuti: “Munyamule umuponye mʼmunda wa Naboti wa ku Yezereeli.+ Kumbukira kuti iwe ndi ine tinkabwera pambuyo pa Ahabu bambo ake, aliyense atakwera pagaleta lake la mahatchi awiri, pa nthawi imene Yehova anamutemberera kuti:+ 26 ‘Yehova wanena kuti: “Ndithu magazi a Naboti+ ndi magazi a ana ake amene ndawaona dzulo, ndidzawabwezera+ pa iwe mʼmunda uwu,” watero Yehova.’ Choncho munyamule umuponye mʼmundamo mogwirizana ndi mawu a Yehova.”+
-