-
Deuteronomo 3:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Mbali yotsala ya dera la Giliyadi ndi Basana yense amene anali mu ufumu wa Ogi ndinaipereka kwa hafu ya fuko la Manase.+ Dera lonse la Arigobi, limene ndi mbali ya Basana linkadziwika kuti ndi dziko la Arefai.
14 Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri ndi a Amaakati.+ Midzi ya ku Basana imeneyo anaipatsa dzina lofanana ndi lake lakuti, Havoti-yairi*+ ndipo imadziwika ndi dzina limeneli mpaka pano. 15 Makiri ndinamupatsa dera la Giliyadi.+ 16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni.
-
-
Deuteronomo 28:63Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
63 Mofanana ndi mmene Yehova anasangalalira kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuchititsa kuti muchuluke, Yehova adzasangalalanso kuti akuwonongeni nʼkukufafanizani, ndipo mudzatheratu mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.
-
-
Yoswa 13:8-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa fuko la Rubeni ndi kwa fuko la Gadi, kutsidya lakumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano.+ 9 Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakatikati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwera a Medeba mpaka kukafika ku Diboni. 10 Anawapatsanso mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori imene inkalamulira ku Hesiboni, mpaka kumalire ndi Aamoni.+ 11 Anapatsidwanso Giliyadi, dera la Agesuri, la Amaakati,+ phiri lonse la Herimoni ndi dera lonse la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12 Mafukowa anapatsidwanso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei. (Mfumu Ogi inali mmodzi mwa Arefai otsala.)+ Mose anagonjetsa anthu onsewa nʼkuwathamangitsa.+
-