-
2 Mbiri 28:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu nʼkulanda mzinda wa Beti-semesi,+ wa Aijaloni+ ndi wa Gederoti. Analandanso mzinda wa Soko ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira komanso wa Gimizo ndi midzi yake yozungulira, ndipo anayamba kukhala kumeneko. 19 Yehova anatsitsa Ayuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera Ayuda kuchita makhalidwe oipa zomwe zinachititsa kuti achite zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.
-