2 Mbiri
28 Ahazi+ anakhala mfumu ali ndi zaka 20 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+ 2 Koma anayenda mʼnjira za mafumu a Isiraeli+ ndipo anafika mpaka popanga zifaniziro zachitsulo+ za Abaala. 3 Kuwonjezera pamenepo, Ahazi anapereka nsembe yautsi mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu.* Iye anawotcha ana ake pamoto+ potsatira zinthu zonyansa zimene ankachita anthu a mitundu ina+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli. 4 Komanso ankapereka nsembe zautsi ndi nsembe zina pamalo okwezeka,+ pamapiri ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+
5 Choncho Yehova Mulungu wake anamʼpereka mʼmanja mwa mfumu ya Siriya+ moti Asiriya anamʼgonjetsa ndipo anagwira anthu ambiri nʼkupita nawo ku Damasiko.+ Komanso Mulungu anachititsa kuti Ahazi agonjetsedwe ndi mfumu ya Isiraeli yomwe inapha asilikali ambirimbiri a Ahaziyo. 6 Peka+ mwana wa Remaliya anapha anthu 120,000 ku Yuda tsiku limodzi ndipo onsewa anali amuna olimba mtima. Iwo anaphedwa chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo.+ 7 Kuwonjezera pamenepo, Zikiri msilikali wa fuko la Efuraimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu mkulu wapanyumba ya mfumu ndiponso Elikana, wachiwiri kwa mfumu. 8 Komanso Aisiraeli anagwira abale awo okwana 200,000 nʼkuwatenga. Pa anthu ogwidwawo panali azimayi komanso ana aamuna ndi aakazi. Anatenganso zinthu zawo zambiri nʼkupita nazo ku Samariya.+
9 Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi. Iye anapita kukakumana ndi asilikali omwe ankabwerera ku Samariya nʼkuwauza kuti: “Tamverani! Yehova Mulungu wa makolo anu wapereka Ayuda mʼmanja mwanu+ chifukwa chakuti anawakwiyira kwambiri ndipo inuyo mwawapha mutakwiya ndipo mkwiyowo wafika mpaka kumwamba. 10 Tsopano mukufuna kuti anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale antchito anu aamuna ndi aakazi.+ Kodi mʼmesa inunso muli ndi mlandu kwa Yehova Mulungu wanu? 11 Tsopano ndimvereni ndipo bwezani abale anu amene mwawagwirawa, chifukwa Yehova wakukwiyirani kwambiri.”
12 Zitatero, amuna ena omwe anali atsogoleri a anthu a fuko la Efuraimu omwe ndi Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu ndi Amasa mwana wa Hadilai anadzudzula asilikali amene anabwera kuchokera kunkhondowo. 13 Iwo anawauza kuti: “Musabweretse kuno anthu amene mwawagwirawo chifukwa tikhala ndi mlandu kwa Yehova. Zimene mukufuna kuchitazi, ziwonjezera machimo athu ndiponso mlandu wathu. Tili kale ndi mlandu waukulu, ndipo Mulungu wakwiyira kwambiri Isiraeli.” 14 Choncho asilikaliwo anasiya anthu aja ndiponso zinthu zimene anatenga+ zija mʼmanja mwa akalonga ndi anthu onse amene anasonkhana pamenepo. 15 Kenako amuna amene anachita kusankhidwa powatchula mayina ananyamuka nʼkutenga anthu ogwidwawo. Anthu onse amene sanavale* anawapatsa zovala kuchokera pa zinthu zimene zinabwera ndi asilikali zija. Anawapatsanso nsapato, chakudya, zakumwa komanso mafuta kuti adzole. Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene ankayenda movutikira anamukweza pabulu. Atatero anawatenga nʼkupita nawo ku Yeriko, kumzinda wa mitengo ya kanjedza, kufupi ndi abale awo. Kenako iwo anabwerera ku Samariya.
16 Pa nthawi imeneyo, Mfumu Ahazi anapempha mafumu a Asuri kuti adzamuthandize.+ 17 Aedomu anabweranso nʼkudzaukira Ayuda ndipo anagwira anthu nʼkuwatenga. 18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu nʼkulanda mzinda wa Beti-semesi,+ wa Aijaloni+ ndi wa Gederoti. Analandanso mzinda wa Soko ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira komanso wa Gimizo ndi midzi yake yozungulira, ndipo anayamba kukhala kumeneko. 19 Yehova anatsitsa Ayuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera Ayuda kuchita makhalidwe oipa zomwe zinachititsa kuti achite zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.
20 Patapita nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kwa iye ndipo anangomuwonjezera mavuto+ mʼmalo momulimbikitsa. 21 Ahazi anali atatenga zinthu za mʼnyumba ya Yehova, za mʼnyumba ya mfumu+ ndi zamʼnyumba za akalonga nʼkuzipereka ngati mphatso kwa mfumu ya Asuri, koma zimenezi sizinamuthandize. 22 Ndipo pa nthawi imene Mfumu Ahazi ankakumana ndi mavuto, anawonjezera kuchita zosakhulupirika kwa Yehova. 23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko+ imene inamugonjetsa,+ ndipo anati: “Milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza, choncho ndipereka nsembe kwa milunguyi kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inachititsa kuti iye ndi Aisiraeli onse akumane ndi mavuto. 24 Kuwonjezera pamenepo, Ahazi anasonkhanitsa ziwiya zamʼnyumba ya Mulungu woona+ nʼkuziphwanyaphwanya. Komanso anatseka zitseko za nyumba ya Yehova.+ Kenako anadzimangira maguwa ansembe mʼmakona onse a mu Yerusalemu. 25 Anamanga malo okwezeka operekera nsembe zautsi kwa milungu ina+ mʼmizinda yonse ya Yuda ndipo anakwiyitsa Yehova Mulungu wa makolo ake.
26 Nkhani zina zokhudza Ahazi ndiponso zimene anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Yuda ndi Isiraeli.+ 27 Kenako Ahazi, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mumzinda wa Yerusalemu. Iye sanaikidwe mʼmanda a mafumu a Isiraeli.+ Ndiyeno Hezekiya mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.